Kale kale ndili ndi agogo, panali chinthu China chake chosayiwalika chomwe chinkachitika: miyambi ndi nthano
Nthano:
Kalulu ndi chule
Tsiku lina Kalulu ndi Chule adapita kokaba ndipo adagwirizana kuti wina asakawulure.
Atafika ku nyumba, Kalulu adadabwa kuwona a Chule pa khosi pali dyoko dyoko, iye adayesa kuti Chule akufuna kuulula posadziwa kuti chinali chikhalidwe chake.
Kalulu: Achule bwanji?
Chule: basi
Kalulu: pakhosipo dyoko dyokoyo bwanji? Mufuna muwulule?
Chule: Aaaa sindiwulula
Ndipo Kalulu anafusa izi mobwereza bwereza mpaka adamukayikila ndikuwagwira onse awiri. Powapanikiza adawulula kuti anakaba.
Miyambi:
Kalipo kalipo ntengo sugwa okha.
Mau wa akulu akoma akagonera.
Wakutsina khutu ndi m'nasi.
Chigololo ndi mwini thako.
Kandinverere adakanena za m'maluwa.
Ichi nchiyani nkulinga muli awiri.
Kali kokha nkanyama, tili tiwiri ntiwanthu.
Dziko ndi anthu thengo ndi nambala.
Chifundo chidaphetsa nkhwali.
Ichi chakoma Ichi chakoma fisi adagwa m'chagada.
Mapanga awiri avumbwitsa.
Mwana wa nzako ndi wako yemwe ukachenjera manja udya naye.
Kandikumbire adankanacho.
Ukayendera nzengo usamati asakhwi afumbula.
Zina ukawona kamba anga mwala
Nsonkhe nsonkhe adadzala thumba.
Nkhitchini mwa mwini saotchera mbewa.
Kwa nzako kuli nchifundo
China nchina nkhwani sawotchera, djekete sapisira
Khoswe wapadenga adawululutsa wa padzala.
Kuyenda awili simantha.
Chala sichiloza mwini.
Chozemba chidakumana nchokwawa adachikoka djekete.
Dala limagonetsa munda.
Dzimbu limalanditsa munda.
Pano mpathu amagonetsa m'njala.
Tsoka sasimba.
Kunja nkumpheto sikuchedwa kusintha.
Mbewa ya manyazi inafera kuuna.
Padakafunda adadyiwitsa galu.
Anthu amuna nkabudula amathera moyenda.
Ukakwera pa nsana pa njovu usamati kulibe mame.
Kati delu kadaopsa mlenje.
Wadabwa Chule mmadzi muli mwake .